7 Anthu akumeneko ankamufunsafunsa za mkazi wake, ndipo iye ankawayankha kuti, “Ndi mchemwali wanga ameneyu.”+ Ankaopa kunena kuti, “Ameneyu ndi mkazi wanga,” chifukwa anati: “Anthu a kuno akhoza kundipha chifukwa cha Rabeka,” pakuti mkaziyo anali wokongola mochititsa kaso.+