-
Luka 17:29-31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Koma tsiku limene Loti anatuluka mu Sodomu, kumwamba kunagwa moto ndi sulufule ngati mvula nʼkuwononga anthu onse.+ 30 Zidzakhalanso chimodzimodzi pa tsikulo, pamene Mwana wa munthu adzaonekere.+
31 Pa tsiku limenelo, munthu amene adzakhale padenga la nyumba koma katundu wake ali mʼnyumba, asadzatsike kukatenga katundu wakeyo. Chimodzimodzinso munthu amene adzakhale ali mʼmunda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya mʼmbuyo.
-