44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+