33 Tsiku lililonse limene mudzabwere kudzaona malipiro anga, mudzaona chilungamo changa. Mukadzapeza mbuzi iliyonse yaikazi yopanda mathothomathotho kapena mawangamawanga, ndi nkhosa iliyonse yaingʼono yamphongo yomwe si yabulauni ili ndi ine, imeneyo ndiye kuti ndaba.”