42 Koma nkhosazo zikakhala zofooka, iye sankaika timitengo tija momwera madzimo. Choncho nthawi zonse nkhosa zofooka zinkakhala za Labani koma zamphamvu zinkakhala za Yakobo.+
43 Yakobo anapeza chuma chambiri. Iye anali ndi ziweto zambiri, antchito aakazi ndi aamuna komanso ngamila ndi abulu.+