31 Dzuwa linali litatuluka pamene Yakobo ankachoka ku Penueli, koma ankayenda motsimphina.+ 32 Nʼchifukwa chake mpaka pano, ana a Isiraeli sadya mtsempha wa pamalo amene fupa la ntchafu limalumikizana ndi chiuno, chifukwa ndi umene munthu uja anagwira polimbana ndi Yakobo.