18 Atachoka ku Padani-aramu,+ Yakobo anafika bwino kumzinda wa Sekemu,+ mʼdziko la Kanani.+ Atafika, anamanga msasa pafupi ndi mzindawo. 19 Kenako anagula malo ndipo anamangapo tenti. Anawagula ndi ndalama zasiliva 100, kwa ana a Hamori, bambo ake a Sekemu.+