25 Ndiyeno abale akewo anakhala pansi kuti adye chakudya. Koma atayangʼana, anaona gulu la Aisimaeli+ amene ankachokera ku Giliyadi. Ngamila zawo zinali zitanyamula zinthu zonunkhira monga labidanamu, basamu komanso makungwa a utomoni wonunkhira.+ Iwo anali pa ulendo wopita ku Iguputo.