Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 31:2-5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Inetu ndasankha* Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndidzamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse, 4 kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 5 waluso losema miyala ndi kupanga zoikamo miyala+ komanso wodziwa kupanga chilichonse chamatabwa.+

  • Ekisodo 35:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Kenako Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova wasankha Bezaleli, mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+

  • Ekisodo 36:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 “Bezaleli adzagwire ntchito limodzi ndi Oholiabu komanso mwamuna aliyense waluso* amene Yehova wamupatsa nzeru ndi kuzindikira kuti adziwe mmene angagwirire ntchito zonse zopatulika mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”+

  • Ekisodo 37:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Kenako Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+

  • 2 Mbiri 1:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Guwa lansembe lakopa*+ limene Bezaleli+ mwana wa Uri mwana wa Hura anapanga, anali ataliika patsogolo pa chihema chopatulika cha Yehova. Ndipo Solomo ndi mpingowo ankapemphera patsogolo pa guwalo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena