15 Pofika pano ndikanakhala nditatambasula kale dzanja langa nʼkupha iweyo komanso anthu ako ndi mliri woopsa, ndipo ndikanakufafanizani padziko lapansi. 16 Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+