-
Ekisodo 18:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno Yetero anati: “Yehova atamandike, amene anakupulumutsani ku Iguputo ndiponso kwa Farao, amenenso analanditsa anthuwa kwa Aiguputo omwe ankawazunza. 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse,+ chifukwa cha zimene anachitira anthu amene ankachita zinthu modzikuza pamaso pa anthu ake.”
-