-
Numeri 11:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo ankaoneka ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi. 8 Anthuwo ankamwazikana kukatola manawo. Akatero, ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo. Kenako ankawawiritsa mumphika, kapena kuwapanga makeke ozungulira+ ndipo ankakoma ngati keke yotsekemera yothira mafuta.
-