-
Ekisodo 24:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kwa Aisiraeli amene ankaona zimenezi, ulemerero wa Yehova unkaoneka ngati moto wolilima pamwamba pa phiri.
-
-
2 Mbiri 7:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Solomo atangomaliza kupemphera,+ moto unatsika kuchokera kumwamba+ nʼkutentha nsembe yopsereza ndiponso nsembe zina ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza nyumbayo.+ 2 Ansembe sanathe kulowa mʼnyumba ya Yehova chifukwa ulemerero wa Yehova unadzaza nyumba ya Yehova.+ 3 Aisiraeli onse ankaonerera pamene moto unkatsika ndiponso pamene ulemerero wa Yehova unali pamwamba pa nyumbayo. Ataona zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi ndipo anayamika Yehova, “chifukwa iye ndi wabwino ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”
-