-
Levitiko 6:2-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 “Munthu akachimwa ndipo wachita mosakhulupirika kwa Yehova+ ponamiza mnzake pa chinthu chimene anamusungitsa,+ kapena chimene anamubwereka, kapena wamubera mnzake, kapena wamuchitira chinyengo, 3 kapena watola chinthu chotayika koma akukana kuti sanachitole, ndipo ngati walumbira monama pa tchimo lililonse limene angachite,+ azichita izi: 4 Ngati wachimwa ndipo wapalamula mlandu, azibweza zinthu zimene anabazo, kapena zinthu zimene analanda mwachinyengo, kapena chimene anamʼsungitsa, kapena chinthu chotayika chimene anatola, 5 kapena chilichonse chimene analumbira monama. Azibweza chinthucho+ nʼkuwonjezerapo limodzi mwa magawo ake 5. Azibweza zimenezi kwa mwiniwake pa tsiku limene wapezeka kuti ndi wolakwa.
-