-
Levitiko 25:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Mʼbale wanu akasauka pakati panu ndipo sangathe kudzisamalira, muzimuthandiza+ ngati mmene mungathandizire mlendo wokhala pakati panu,+ kuti nayenso akhale ndi moyo. 36 Musamalandire chiwongoladzanja kapena kupezerapo phindu+ pa iye.* Muziopa Mulungu wanu+ ndipo mʼbale wanu azikhala ndi moyo pakati panu.
-
-
Luka 6:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Komanso, ngati mumakongoza popanda chiwongoladzanja kwa okhawo amene mukuyembekezera kuti adzabweza ngongoleyo, mudzapindula chiyani?+ Ochimwanso amakongoza ochimwa anzawo popanda chiwongoladzanja, kuti adzawabwezere zomwezo. 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino ndi kukongoza popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse.+ Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wamʼmwambamwamba, chifukwa iye ndi wokoma mtima kwa osayamika ndi kwa oipa.+
-