-
Deuteronomo 9:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Nditayangʼana, ndinaona kuti mwachimwira Yehova Mulungu wanu. Munali mutadzipangira mwana wa ngʼombe wachitsulo.* Munali mutapatuka mofulumira panjira imene Yehova anakulamulani kuti muziyendamo.+ 17 Choncho ndinatenga miyala iwiriyo nʼkuiponya pansi mwamphamvu ndi manja anga, ndipo ndinaiswa inu mukuona.+
-