18 Zitatero ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinkadya chakudya kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita pochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova nʼkumukhumudwitsa.