-
Levitiko 9:18-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Ndiyeno Aroni anapha ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yamgwirizano yoperekera anthuwo. Kenako ana ake anamupatsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mbali zonse za guwa lansembe.+ 19 Koma mafuta a ngʼombeyo,+ mchira wa mafuta wa nkhosa, mafuta okuta ziwalo za mʼmimba, impso ndi mafuta apachiwindi,+ 20 ana a Aroni anaika mafuta amenewo pamwamba pa zidale za nyamazo. Kenako anawotcha mafutawo paguwa lansembe.+
-