13 “Uuze Aisiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti mukusunga masiku anga a sabata.+ Chimenechi ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu mʼmibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.
8 Muzimuona kuti ndi woyera+ chifukwa ndi amene amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu, chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+
23 Mulungu wamtendereyo akupatuleni kuti muchite utumiki wake. Ndipo pa mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu komanso thupi lanu, zikhale zopanda chilema kapena cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+