5 Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi nʼkumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mwamuna wochokera mʼbanja lina. Mlamu wake azipita kwa iye nʼkukamutenga kukhala mkazi wake, ndipo azichita ukwati wa pachilamu.+