-
Rute 4:4-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Ndiye ine ndaganiza zoti ndikuuze kuti, ‘Ugule malowo pamaso pa anthu ndiponso pamaso pa akulu a mzindawu.+ Ngati ukufuna kuwawombola, awombole. Koma ngati sukufuna undiuze, chifukwa iweyo ndiye woyenera kuwombola malowo ndipo pambuyo pako pali ineyo.’” Iye anayankha kuti: “Ndiwombola ineyo.”+ 5 Kenako Boazi anati: “Ukadzagula malowo kwa Naomi, ndiye kuti wagulanso kwa Rute wa ku Mowabu, amene mwamuna wake anamwalira, kuti dzina la mwamuna wakeyo libwerere pacholowa chake.”+ 6 Wowombolayo atamva zimenezi anati: “Sinditha kuwombola, chifukwa ndingawononge cholowa changa. Inuyo wombolani mʼmalo mwa ine, chifukwa ine sinditha kuwombola.”
-