1 Mbiri 22:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo*+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+ Salimo 29:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+ Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendere.+ Hagai 2:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 ‘Ulemerero wa nyumba yatsopanoyi udzakhala waukulu kuposa wa nyumba yoyamba ija,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. ‘Ndipo ndidzakupatsani mtendere pamalo ano,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”
9 Tamvera, udzabereka mwana.+ Mwana ameneyo adzakhala munthu wokonda mtendere ndipo ndidzachititsa kuti azikhala mwamtendere komanso asamavutitsidwe ndi adani ake omuzungulira.+ Nʼchifukwa chake dzina lake adzakhala Solomo*+ ndipo mʼmasiku ake ndidzapatsa Aisiraeli bata ndi mtendere.+
9 ‘Ulemerero wa nyumba yatsopanoyi udzakhala waukulu kuposa wa nyumba yoyamba ija,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. ‘Ndipo ndidzakupatsani mtendere pamalo ano,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”