Ekisodo 24:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Kenako anatenga buku la pangano nʼkuwerengera anthuwo mokweza.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+ Deuteronomo 31:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ Aheberi 8:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 ‘Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ Popeza sanapitirize kusunga pangano langalo, ndinasiya kuwasamalira,’ akutero Yehova.”*
7 Kenako anatenga buku la pangano nʼkuwerengera anthuwo mokweza.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+
16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+
9 ‘Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ Popeza sanapitirize kusunga pangano langalo, ndinasiya kuwasamalira,’ akutero Yehova.”*