Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Anthu adzachita mantha akadzaona zimene zakuchitikirani ndipo mudzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene Yehova akukuthamangitsirani.+

  • Deuteronomo 29:22-24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Mʼbadwo wa mʼtsogolo wa ana anu ndiponso mlendo wochokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi matenda amene Yehova wabweretsa mʼdzikoli—* 23 akadzaona kuti dziko lonse lawonongedwa ndi sulufule, mchere ndi kutentha, moti mʼdzikomo simungadzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, ndipo likuoneka ngati Sodomu ndi Gomora,+ Adima ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga ndi ukali komanso mkwiyo wake—* 24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’

  • Yeremiya 18:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chochititsa mantha+

      Komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+

      Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyangʼanitsitsa mwamantha ndipo adzapukusa mutu wake.+

  • Maliro 2:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba mʼmanja monyoza.+

      Akuimba mluzu modabwa+ ndipo akupukusira mitu yawo mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti:

      “Kodi uwu ndi mzinda umene ankaunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri ndipo anthu padziko lonse lapansi amasangalala nawoʼ?”+

  • Ezekieli 5:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Udzakhala chinthu chimene anthu azidzachinyoza komanso kuchichitira chipongwe.+ Zimene zidzakuchitikire zidzakhala chenjezo ndipo zidzabweretsa mantha kwa anthu a mitundu yokuzungulira. Zimenezi zidzachitika ndikadzapereka chiweruzo kwa iwe komanso kukulanga mokwiya ndiponso mwaukali. Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena