-
Levitiko 11:21-24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Pa tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso timayenda ndi miyendo yonse 4, mungathe kudya tizilombo tokhato timene tili ndi miyendo iwiri italiitali yolumphira. 22 Tizilombo timene mungadye ndi iti: mitundu yosiyanasiyana ya dzombe loyenda mitunda italiitali, mitundu ina ya dzombe lodyedwa,+ nkhululu ndi ziwala. 23 Koma tizilombo tina tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu. 24 Zamoyo zimenezi nʼzimene mungadzidetse nazo. Aliyense wokhudza zamoyo zimenezi zitafa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.+
-
-
Deuteronomo 14:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Musamadyenso nkhumba chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake kapena kuikhudza ikafa.
-