-
Levitiko 12:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kumʼphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera pa kukha magazi kwake. Limeneli ndi lamulo lokhudza mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi. 8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi izikhala ya nsembe yopsereza, inayo izikhala ya nsembe yamachimo. Akatero wansembe adzamuphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera.’”
-
-
Levitiko 14:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu. 22 Komanso azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, mogwirizana ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+
-
-
Levitiko 15:13-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndiyeno munthuyo akachira nthenda yake yakukhayo, pazipita masiku 7 kuti akhale woyera. Kenako azichapa zovala zake nʼkusamba madzi otunga kumtsinje, ndipo iye adzakhala woyera.+ 14 Pa tsiku la 8 azitenga njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda+ ndipo azibwera nazo pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako, nʼkuzipereka kwa wansembe. 15 Ndiyeno wansembe azipereka nsembe mbalamezo, imodzi monga nsembe yamachimo ndipo inayo monga nsembe yopsereza. Wansembe azimuphimbira machimo pamaso pa Yehova chifukwa cha nthenda yake yakukhayo.
-