-
Levitiko 6:14-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tsopano lamulo la nsembe yambewu+ ndi ili: Ana a Aroni azibweretsa nsembeyi pamaso pa Yehova patsogolo pa guwa lansembe. 15 Mmodzi mwa iwo azitapako ufa wosalala wa nsembe yambewu kudzaza dzanja limodzi komanso azitengako mafuta ake ndi lubani yense amene ali pansembe yambewuyo. Akatero, aziziwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 16 Aroni ndi ana ake azidya zotsala za nsembe imeneyi.+ Azipanga mkate wopanda zofufumitsa ndi kudya mkatewo mʼmalo oyera. Aziudyera mʼbwalo la chihema chokumanako.+
-