-
Genesis 28:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Yakobo analonjeza kuti: “Mulungu akapitiriza kukhala nane komanso kunditeteza pa ulendo wangawu, ndiponso akadzandipatsa chakudya ndi zovala, 21 komanso ndikadzabwerera mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga. 22 Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatse, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi.”
-