-
Numeri 32:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Kenako iwo anapitanso kwa iye nʼkunena kuti: “Mutilole timange makola amiyala a ziweto zathu kunoko ndi mizinda ya ana athu.
-
-
Numeri 32:34-38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Ndipo ana a Gadi anamanga* mizinda ya Diboni,+ Ataroti,+ Aroweli,+ 35 Atiroti-sofani, Yazeri,+ Yogebeha,+ 36 Beti-nimira+ ndi Beti-harana.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri komanso inali ndi makola a ziweto amiyala. 37 Ana a Rubeni anamanga mizinda ya Hesiboni,+ Eleyale,+ Kiriyataimu,+ 38 Nebo,+ Baala-meoni,+ ndi Sibima. Mayina a mizindayi anawasintha, nʼkuipatsa mayina ena atsopano.
-