Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 3:16, 17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni. 17 Ndinawapatsanso Araba, mtsinje wa Yorodano ndi malo amʼmbali mwa mtsinjewo, kuchokera ku Kinereti* mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere* imene ili mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga, chakumʼmawa.+

  • Yoswa 11:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Yabini mfumu ya ku Hazori atangomva zimenezi, anatumiza uthenga woitanitsa Yobabi mfumu ya ku Madoni,+ mfumu ya ku Simironi ndi mfumu ya ku Akasafu.+ 2 Anatumizanso uthenga kwa mafumu amʼdera lamapiri kumpoto, mafumu amʼchigwa* chakumʼmwera kwa Kinereti, mafumu a ku Sefela ndiponso mafumu okhala mʼmapiri a Dori+ kumadzulo.

  • Luka 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Nthawi inayake, gulu la anthu linkamvetsera pamene Yesu ankaphunzitsa mawu a Mulungu mʼmphepete mwa nyanja ya Genesarete*+ ndipo anthuwo ankamupanikiza.

  • Yohane 6:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pambuyo pa zimenezi, Yesu anawolokera kutsidya lina la nyanja ya Galileya,* kapena kuti nyanja ya Tiberiyo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena