Genesis 9:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene adzakupheni* ndidzamupatsa chilango. Ngati chamoyo chilichonse chapha munthu, chamoyocho chidzaphedwanso. Ndipo munthu aliyense wochotsa moyo wa mʼbale wake, ndidzamupatsa chilango.+ Ekisodo 21:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Aliyense amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa.+ Levitiko 24:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Munthu aliyense amene wapha munthu, nayenso aziphedwa ndithu.+ Deuteronomo 19:11, 12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Koma ngati munthu amadana ndi mnzake+ ndipo wamubisalira panjira nʼkumuvulaza kwambiri mpaka mnzakeyo kufa, iye nʼkuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu amumzinda wakwawo azimuitanitsa kuchokera kumeneko nʼkumupereka mʼmanja mwa wobwezera magazi ndipo azimupha.+
5 Kuwonjezera pamenepo, aliyense amene adzakupheni* ndidzamupatsa chilango. Ngati chamoyo chilichonse chapha munthu, chamoyocho chidzaphedwanso. Ndipo munthu aliyense wochotsa moyo wa mʼbale wake, ndidzamupatsa chilango.+
11 Koma ngati munthu amadana ndi mnzake+ ndipo wamubisalira panjira nʼkumuvulaza kwambiri mpaka mnzakeyo kufa, iye nʼkuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu amumzinda wakwawo azimuitanitsa kuchokera kumeneko nʼkumupereka mʼmanja mwa wobwezera magazi ndipo azimupha.+