30 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31 Ntchito yawo inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ziwiya+ zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼmalo oyerawo, nsalu yotchinga+ komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+