-
2 Samueli 6:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Koma atafika kumalo opunthira mbewu a ku Nakoni, Uza anagwira Likasa la Mulungu woona,+ chifukwa ngʼombe zinatsala pangʼono kuligwetsa. 7 Zitatero Yehova anakwiyira kwambiri Uza ndipo Mulungu woona anamuphera+ pomwepo chifukwa chochita zinthu mopanda ulemu.+ Moti Uza anafera pompo, pafupi ndi Likasa la Mulungu woona.
-