-
Numeri 5:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ngati mwamuna wake akuchita nsanje ndipo akukayikira kuti mkazi wake wachita chigololo nʼkudzidetsa pamene mkaziyo wachitadi chigololo, kapena ngati akuchita nsanje nʼkumakayikira kuti mkazi wake wachita chigololo pamene mkaziyo sanachite, 15 mwamunayo azitenga mkaziyo nʼkupita naye kwa wansembe. Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yokumbutsa cholakwa.
-