-
Ekisodo 18:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli monse kuti akhale atsogoleri a anthu. Anasankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.
-
-
Yoswa 22:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Kenako Aisiraeli anatumiza Pinihasi+ mwana wa wansembe Eleazara, kwa anthu a fuko la Rubeni, la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase, ku Giliyadi. 14 Anamʼtumiza pamodzi ndi atsogoleri 10. Fuko lililonse la Isiraeli linatumiza mtsogoleri mmodzi woimira nyumba ya makolo ake. Mtsogoleri aliyense anali woimira nyumba ya bambo ake pakati pa Aisiraeli masauzande.+
-
-
1 Mbiri 27:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Awa ndi magulu a Aisiraeli amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100+ ndiponso anthu omwe ankatumikira mfumu+ pa nkhani iliyonse yokhudza magulu amenewa. Maguluwa ankasinthanasinthana mwezi uliwonse pa chaka ndipo gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.
-