Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Muzibweretsa kunyumba ya Yehova Mulungu wanu zipatso zoyamba kucha zamʼminda yanu zomwe ndi zabwino kwambiri.+

      Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+

  • Levitiko 27:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Koma zinthu zimene munthu wapereka kwa Yehova monga zinthu zoyenera kuwonongedwa, kuchokera pa katundu wake, sizikuyenera kugulitsidwa kapena kuwomboledwa, kaya ndi munthu, nyama kapena munda. Chinthu chilichonse chimene munthu wapereka kwa Yehova ndi chopatulika koposa.+

  • Levitiko 27:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 Chakhumi chilichonse+ cha zinthu zamʼdzikolo, kaya ndi zokolola zamʼmunda kapena zipatso zamʼmitengo, ndi za Yehova. Chakhumi chimenechi ndi chopatulika kwa Yehova.

  • Numeri 18:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Zinthu izinso zizikhala zako: mphatso zonse za Aisiraeli,+ limodzi ndi nsembe zawo zonse zoyendetsa uku ndi uku+ zimene azipereka. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna komanso ana ako aakazi kuti zikhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.+

  • Numeri 18:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 “Uza Alevi kuti, ‘Muzilandira kwa Aisiraeli chakhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale cholowa chanu.+ Ndipo pa chakhumi chimene muzilandiracho, muzipereka chakhumi kwa Yehova.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena