-
Ekisodo 17:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tsogola ndipo utenge ena mwa akulu a Isiraeli komanso ndodo yako imene unamenya nayo mtsinje wa Nailo.+ Uitenge mʼdzanja lako ndipo uziyenda. 6 Tamvera! Ine ndidzatsogola nʼkukaima pathanthwe ku Horebe. Kumeneko ukamenye thanthwelo ndipo padzatuluka madzi amene anthu adzamwe.”+ Mose anachitadi zomwezo pamaso pa akulu a Isiraeli.
-