5 Musalimbane nawo, chifukwa sindikupatsani mbali iliyonse ya dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha, chifukwa ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+ 6 Mudzawapatse ndalama pa chakudya chimene mudzadye, ndipo mudzapereke ndalama pa madzi amene mudzamwe.+