Numeri 20:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera mʼdziko lake. Zitatero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+ Deuteronomo 2:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Choncho tinadutsa pafupi ndi abale athu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba, Elati ndi Ezioni-geberi.+ Kenako tinatembenuka nʼkudutsa njira ya mʼchipululu cha Mowabu.+ Oweruza 11:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pamene ankadutsa mʼchipululu, analambalala dziko la Edomu+ ndi la Mowabu. Anadutsa chakumʼmawa kwa dziko la Mowabu+ nʼkukamanga misasa mʼchigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu chifukwa Arinoni ndi amene anali malire a Mowabu.+
21 Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera mʼdziko lake. Zitatero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+
8 Choncho tinadutsa pafupi ndi abale athu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba, Elati ndi Ezioni-geberi.+ Kenako tinatembenuka nʼkudutsa njira ya mʼchipululu cha Mowabu.+
18 Pamene ankadutsa mʼchipululu, analambalala dziko la Edomu+ ndi la Mowabu. Anadutsa chakumʼmawa kwa dziko la Mowabu+ nʼkukamanga misasa mʼchigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu chifukwa Arinoni ndi amene anali malire a Mowabu.+