4 Hezekiya ndi amene anachotsa malo okwezeka,+ kugwetsa zipilala zopatulika ndiponso kudula mzati wopatulika.+ Komanso iye anaphwanyaphwanya njoka yakopa imene Mose anapanga,+ chifukwa pa nthawiyi Aisiraeli ankafukiza nsembe yautsi kwa njokayo ndipo inkatchedwa fano la njoka yakopa.