-
Deuteronomo 2:30-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Koma Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni sinatilole kuti tidutse mʼdziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ komanso kuti aumitse mtima wake, nʼcholinga choti amupereke mʼmanja mwanu monga mmene zilili lero.+
31 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndayamba kale kupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+ 32 Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenya nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33 Yehova Mulungu wathu anamupereka kwa ife ndipo tinamugonjetsa limodzi ndi ana ake komanso anthu ake onse. 34 Pa nthawi imeneyo, tinalanda mizinda yake yonse ndi kuwononga mzinda wina uliwonse. Tinapha amuna, akazi ndi ana ndipo sitinasiye munthu aliyense ndi moyo.+ 35 Ziweto zokha nʼzimene tinatenga pamodzi ndi zinthu zimene tinatenga mʼmizinda imene tinalanda.
-
-
Oweruza 11:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Kenako Aisiraeli anatumiza uthenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, ya ku Hesiboni, kuti: “Tingadutse nawo mʼdziko lanu kupita kumalo athu?”+ 20 Koma Sihoni sanakhulupirire kuti Aisiraeli akufuna kungodutsa mʼdziko lake. Choncho Sihoni anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkumanga misasa ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeliwo.+
-