13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.
16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni.