-
Yoswa 12:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Awa ndi mafumu amene Aisiraeli anagonjetsa nʼkulanda madera awo kumʼmawa kwa mtsinje wa Yorodano, kuchokera kuchigwa cha Arinoni+ kukafika kuphiri la Herimoni+ ndi ku Araba konse, chakumʼmawa:+ 2 Sihoni+ mfumu ya Aamori, yemwe ankakhala ku Hesiboni ndipo ankalamulira kuyambira kumzinda wa Aroweli,+ womwe unali mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni+ komanso kuyambira pakatikati pa chigwachi, ndi hafu ya Giliyadi mpaka kukafika kuchigwa cha Yaboki, kumalire ndi Aamoni.
-