-
Genesis 38:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Koma makhalidwe a Ere, mwana woyamba wa Yuda, sanasangalatse Yehova ndipo Yehova anamupha. 8 Yuda ataona zimenezi anauza Onani kuti: “Gona ndi mkazi wa mchimwene wako ndipo ulowe chokolo,* kuti umuberekere ana mchimwene wako.”+ 9 Koma Onani anadziwa kuti anawo sadzakhala ake.+ Choncho, nthawi zonse akagona ndi mkazi wa mʼbale wakeyo, ankataya pansi umuna wake kuti asamuberekere ana mʼbale wakeyo.+ 10 Zimene ankachitazo zinali zoipa pamaso pa Yehova, choncho nayenso anamupha.+
-