18 Samalani kuti pakati panu lero pasapezeke mwamuna, mkazi, banja kapena fuko limene mtima wake wapatuka kusiya Yehova Mulungu wathu nʼkupita kukatumikira milungu ya mitundu inayo,+ kuti pakati panu pasapezeke muzu wotulutsa chipatso chapoizoni komanso chitsamba chowawa.+