12 Mukawawonongatu Aiguputo anena kuti, ‘Anali ndi zolinga zoipa powatulutsa mʼdziko lino. Iye amafuna kuti akawaphe kumapiri nʼkuwafafaniza padziko lapansi.’+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo, ndipo sinthani maganizo anu ofuna kubweretsera anthu anu tsoka limeneli.