14 Abulamu atasiyana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo. 15 Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa zako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+