-
Nehemiya 9:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Ndiyeno munakhaulitsa Farao, atumiki ake onse ndiponso anthu onse amʼdziko lake powaonetsa zizindikiro ndi zodabwitsa.+ Munachita zimenezi chifukwa munadziwa kuti iwo anachita zinthu modzikuza+ kwa makolo athu. Pamenepa munadzipangira dzina lomwe lilipobe mpaka lero.+ 11 Munagawa nyanja pamaso pawo ndipo anadutsa panthaka youma.+ Anthu amene ankawathamangitsa munawaponya pansi pa nyanja ngati mwala woponyedwa mʼmafunde amphamvu.+
-