-
Numeri 6:23-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Mukamadalitsa+ Aisiraeli muziwauza kuti:
24 “Yehova akudalitseni+ ndipo akutetezeni.
25 Yehova asonyeze kuti akusangalala nanu+ ndipo akukomereni mtima.
26 Yehova akuyangʼaneni mokondwera ndipo akupatseni mtendere.”’+
27 Aroni ndi ana ake azigwiritsa ntchito dzina langa podalitsa Aisiraeli+ kuti ine ndiwadalitse.”+
-