-
Levitiko 11:13-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Izi ndi zamoyo zouluka zimene muyenera kuziona kuti ndi zonyansa. Sizikuyenera kudyedwa chifukwa ndi zonyansa: chiwombankhanga,+ nkhwazi, muimba wakuda,+ 14 mphamba wofiira, mtundu uliwonse wa mphamba wakuda, 15 mtundu uliwonse wa khwangwala, 16 nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa, mtundu uliwonse wa kabawi, 17 nkhwezule, chiswankhono, mantchichi, 18 tsekwe, vuwo, muimba, 19 dokowe, mtundu uliwonse wa chimeza, sadzu ndi mleme. 20 Tizilombo tonse timene timapezeka tambiri, tamapiko ndiponso tamiyendo 4, ndi tonyansa kwa inu.
-